Zechariah 14:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mudzapulumuka podzera m'chigwa chimenecho cha pakati pa mapiri. Mudzathaŵa monga m'mene mudaathaŵira nthaŵi ija ya chivomezi pa nthaŵi ya Uziya mfumu ya ku Yuda. Kenaka Chauta, Mulungu wanu, adzabwera pamodzi ndi oyera ake onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mudzathawa kudzera cigwa ca mapiri anga; pakuti cigwa ca mapiri cidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira cibvomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.