Zechariah 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lidzakhala tsiku la kuŵala kokhakokha, osakhala usana, osakhala usiku, chifukwa ndi madzulo omwe kuzidzaŵalabe. Tsiku limene zidzachitike zimenezi ndi Chauta yekha akulidziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbee.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.