Zechariah 14:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo madzi a moyo adzatuluka ku Yerusalemu. Theka la madziwo lidzathira m'nyanja yakuvuma, theka lina lidzathira m'nyanja yakuzambwe. Zimenezi zidzachitika pa nthaŵi yachilimwe ndi yachisanu yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzaturuka ku Yerusalemu; gawo lao lina kumka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kumka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.