Zechariah 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, fuwula ndipo sangalala. Pakuti taona ndikubwera, ndipo ndidzakhala pakati pako,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yimba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndirinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.