Zechariah 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense wokantha inu, wakantha chinthu cha mtengo wapatali zedi kwa Ine.” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa mitundu imene idaagwira anthu ake kukaiwuza uthenga wake wakuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Atatha kundilemekeza wanditumiza kwa anthu a mitundu ina amene anakufunkhani; pakuti aliyense wokhudza inu wakhudza mwanadiso wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lace.