Zechariah 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta ndidzaŵamenya anthuwo ndi dzanja langa, ndipo amene anali akapolo ao, ndiwo amene adzaŵalande chuma chao.” Pamenepo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu Ine ndidzawamenya anthuwo ndi dzanja langa ndipo amene anali akapolo awo ndiye adzawalande zinthu. Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye wandituma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.