Zechariah 3:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'masomphenya Chauta adandiwonetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, ataima pamaso pa mngelo wake, ku dzanja lake lamanja kutaima Satana woti amuimbe mlandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lake lamanja, atsutsana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lace lamanja, atsutsana naye.