Zechariah 3:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo uja adauza omperekeza aja kuti, “Mvekeni nduŵira yabwino.” Motero adamuveka nduŵira yabwino pa mutu, namuvekanso zovala zatsopano. Nthaŵiyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pace. Naika nduwira yoyera pamutu pace, nambveka ndi zobvala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo,