Zechariah 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano imva, iwe Yoswa, mkulu wa ansembe, imvani nanunso ansembe anzakenu, amene muli chizindikiro cha zabwino zimene zidzachitike. Ndidzabwera naye mtumiki wanga wotchedwa dzina loti “Nthambi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo cizindikilo; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.