Zechariah 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawutu mwala umene ndaika pamaso pa Yoswa, mwala umodzi wa mbali zisanu ndi ziŵiri. Mwiniwakene ndidzazokotapo mau, ndidzachotsa machimo a m'dziko lino pa tsiku limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taona, mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzaloca malocedwe ace, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzacotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.