Zechariah 4:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli. (“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona cingwe colungamitsira ciriri m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.