Zechariah 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamufunsanso kuti, “Pambali pa mipopi iŵiri yagolide yodzera mafutayo pali nthambi ziŵiri za mtengo wa olivi, zimenezi zikutanthauza chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamufunsanso kuti, “Kodi nthambi ziwiri za mtengo wa olivi zomwe zili pambali pa mipopi yodzera mafuta iwiri yagolide zikutanthauza chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinayankha kaciwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zirikutsanula zokha mafuta onga golidi mwa misiwe iwiri yagolidi?