Zechariah 4:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikapo nyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, coikapo nyali ca golidi yekha yekha, ndi mbale yace pamwamba pace, ndi nyali zace zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pace;