Zechariah 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mngelo uja adandifunsa kuti “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Chikalata chofutukula chikuuluka, muutali mwake mamita asanu ndi anai, muufupi mwake mamita anai ndi hafu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wace mikono makumi awiri, ndi citando cace mikono khumi.