Zechariah 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira pa dziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lirikuturukira pa dziko lonse; pakuti ali yense wakuba adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi ali yense wakulumbira zonama adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili.