Zechariah 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzalitulutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yake, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yake ndi miyala yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzaliturutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yace, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yace ndi miyala yace.