Zechariah 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidafunsa kuti, “Kodi nchiyani?” Iye adati, “Chimenechi ndi gondolo loyesera, ndipo likutanthauza uchimo wa anthu m'dziko lonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?” Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;