Zechariah 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a cumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.