Zechariah 6:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona zinthu zinanso m'masomphenya: ndidaona magaleta anai akutuluka pakati pa mapiri aŵiri, mapiri ake amkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona magaleta anayi akutuluka pakati pa mapiri awiri, mapiri amkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka magareta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.