Zechariah 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lace ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwace, nadzamanga Kacisi wa Yehova: