Zechariah 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu okhala kutali adzabwera kudzamanga Nyumba ya Chauta. Motero mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse wandituma kwa inu. Zimenezi zidzachitika ngati mumveradi mwachangu Chauta, Mulungu wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akukhala kutari adzafika, nadzamanga ku Kacisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ici cidzacitika ngati mudzamvera mwacangu mau a Yehova Mulungu wanu.