Zechariah 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve cilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wace mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukuru wocokera kwa Yehova wa makamu.