Zechariah 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe amachitira kamvulumvulu, ndidaŵamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu imene iwo sankaidziŵa, ndipo dziko lao lidasanduka chipululu, kotero kuti palibenso wina amene ankayendamo. Choncho dziko lao lokomalo lidasandukadi chipululu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ndidzawabalalitsa ndi kabvumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwa. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.