Zechariah 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wacisanu, ndi wacisanu ndi citatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?