Zechariah 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mpaka nthaŵi imeneyo panalibe wina wolandirapo malipiro pa ntchito kapena wopindulapo pa zoŵeta. Panalibe munthu amene ankadziyendera mwamtendere, chifukwa cha adani, popeza kuti anthu onse ndidaaŵayambanitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakuturuka, kapena wakulowa, cifukwa ca wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzace.