Zechariah 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Adzabzala mwamtendere, mpesa udzabala zipatso zake, ndipo nthaka idzabereka kwambiri. Mvula idzagwa kuchokera kumwamba. Madalitso onseŵa ndidzaŵapatsa otsala mwa anthuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapata mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zace, ndi nthaka idzapatsa zobala zace, ndi miyamba Idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, cikhale colowa cao.