Zechariah 8:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mabanja a Yuda ndi Israele, kale munali chizindikiro cha matemberero pakati pa mitundu ina ya anthu. Koma tsopano ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala chizindikiro cha madalitso. Musaope, limbani mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika kuti, monga munali cotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israyeli, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala codalitsa naco; musaope, alimbike manja anu.