Zechariah 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Paja ndidaatsimikiza mtima kuti ndikuwonongeni, chifukwa chakuti makolo anu adaandikwiyitsa, ndipo sindidafune kukhululuka. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndil nalingirira kucitira inu coipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;