Zechariah 8:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wacinai, ndi kusala kwa mwezi wacisanu, ndi kusala kwa mwezi wacisanu ndi ciwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda cimwemwe ndi cikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; cifukwa cace kondani coonadi ndi mtendere.