Zechariah 8:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, pa masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a zilankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nao, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu: Kudzacitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.