Zechariah 8:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Ngakhale ziwoneke ngati zosatheka kwa anthu a m'fuko limeneli amene adzatsale nthaŵi imeneyo, kodi zimenezi zidzakhalanso zosatheka ndi kwa Ine ndemwe?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu: Cikakhala codabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi cidzakhalanso codabwitsa pamaso panga? ati Yehova wa makamu.