Zechariah 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a Chauta akudzudzula dziko la Hadaraki, ndiponso mzinda wa Damasiko. Paja mizinda yonse ya ku Aramu njake ya Chauta, chimodzimodzi ngati mafuko onse a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki ndi mzinda wa Damasiko pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli ali pa Yehova—
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pace; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israyeli;