Zechariah 9:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu. Uta wankhondo adzauthyola. Mfumu yanu idzachititsa mtendere pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku mathero a dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa m'Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu, ndipo uta wankhondo udzathyoka. Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu. Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.