Zechariah 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Tsono kunena za inu, chifukwa cha chipangano changa ndi inu, chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza, ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi anthu anu amene ali ngati akapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine, ndidzamasula amʼndende ako, ndidzawatulutsa mʼdzenje lopanda madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwenso, cifukwa ca mwazi wa pangano lako ndinaturutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.