Zechariah 9:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzakoka Yuda ngati uta wanga, Efuremu adzakhala ngati muvi wake. Ndidzatenga ana ako, iwe Ziyoni, kuti alimbane ndi ana ako, iwe Grisi; ndidzakugwira ngati lupanga la wankhondo wamphamvu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga, ndipo Efereimu ndiye muvi wake. Ndidzadzutsa ana ako iwe Ziyoni, kulimbana ndi ana ako iwe Grisi, ndipo ndidzakusandutsa iwe lupanga la munthu wankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efraimu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.