Zechariah 9:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adzaonekera anthu ake, ndipo mivi yake adzaiponya ngati zing'aning'ani. Ambuye Chauta adzaliza lipenga, ndipo adzayenda m'kamvulumvulu wochokera kumwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akavumbulu a kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake; mivi yake idzangʼanima ngati chingʼaningʼani. Ambuye Yehova adzaliza lipenga; ndipo adzayenda mu mkuntho wochokera kummwera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi mubvi wace udzaturuka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akabvumvulu a kumwela.