Zechariah 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse adzakhala chishango chao. Iwowo adzapambana ndi kugonjetsa adani ao poponya miyala chabe. Adzamwa magazi ao nkumafuula ngati okhuta vinyo. Magaziwo adzachita kuyenderera ngati magazi a nsembe, othira ndi mkhate pa guwa popembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza. Iwo adzawononga ndipo adzagonjetsa ndi miyala ya legeni. Adzamwa magazi ndi kubangula ngati amwa vinyo; magazi adzayenderera ngati a mʼmbale yowazira magazi pa ngodya za guwa lansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu adzawacinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzacita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngondya za guwa la nsembe.