Zechariah 9:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa, pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa. M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa pakuti anthu ake ali ngati nkhosa. Adzanyezimira mʼdziko lake ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ace; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lace.