Zechariah 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Asikeloni nawonso udzaziwona zimenezo, nkuchita mantha. Gaza adzakhwinyata ndi mantha, Ekeroninso chimodzimodzi, chifukwa zimene ankayembekeza zidzasokonezeka. Mfumu ya ku Gaza idzachotsedwa, ku Asikeloni kudzakhala kopanda anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha; Gaza adzanjenjemera ndi ululu, chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu. Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asikeloni adzaciona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekroni, pakuti ciyembekezo cace cacitidwa manyazi; ndipo mfumu idzatayika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.