Zechariah 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ake sadzadyanso nyama yamagazi, kapena nyama yoletsedwa iliyonse. Otsala onse adzakhala anthu anga, adzasanduka ngati fuko la ku Yuda. Nawonso Aekeroni adzakhala ngati Ayebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko m'Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo, chakudya choletsedwa mʼmano mwawo. Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu, adzasanduka atsogoleri mu Yuda, ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzacotsa mwazi wace m'kamwa mwace, ndi zonyansa zace pakati pa mano ace; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkuru wa pfuko m'Yuda, ndi Ekroni ngati Myebusi.