Zephaniah 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo kulira kwakukulu kudzamveka ku Chipata cha Msika wa Nsomba; kulira kwakukuluko kudzamveka ku chigawo cham'kati cha mzinda wa Yerusalemu; kudzamvekanso kugunda kuchokera ku mapiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera kuchipata chansomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova, “Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba, kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano, ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira locokera ku cipata cansomba, ndi kucema kocokera ku dera laciwiri, ndi kugamuka kwakukuru kocokera kuzitunda.