Zephaniah 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale, ndipo ndidzaŵalanga anthu ongokhala khale ngati vinyo wosakhutchumula, amene mumtima mwao amati, ‘Chauta sadzachitapo chabwino, kapena kuchitapo choipa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale ndi kulanga onse amene sakulabadira, amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa, amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse, chabwino kaya choyipa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sacita cokoma, kapena kucita coipa.