Zephaniah 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu otereŵa chuma chao adani adzachifunkha, nyumba zao adzaziphwasula. Adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo. Adzabzala mphesa, koma sadzamwa vinyo wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzanka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wace.