Zephaniah 1:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lalikulu la Chauta lili pafupi, layandikira ndipo likudza mofulumira. Tsikulo kubwera kwake nkopweteka, ngakhale ankhondo amphamvu omwe akulira pamenepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lalikulu la Yehova layandikira, layandikira ndipo lifika msanga. Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa, ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lalikuru la Yehova liri pafupi, liri pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.