Zephaniah 1:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale siliva wao kapena golide wao sadzatha kuŵaombola, tsiku la mkwiyo wa Chautalo. Ukali wake wotentha ngati moto, udzapsereza dziko lonse, ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale siliva wao, ngakhale golidi wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yace; pakuti adzacita cakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.