Zephaniah 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzafafaniziratu anthu ndi nyama zomwe. Ndidzaononga mbalame zamumlengalenga ndi nsomba zam'nyanja. Ndidzagwetsa anthu ochimwa. Ndidzafafaniziratu mtundu wa anthu kuti usaonekenso pa dziko lapansi,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe; ndidzawononga mbalame zamlengalenga ndi nsomba za mʼnyanja. Ndidzawononga anthu oyipa, ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwacotsa panthaka, ati Yehova.