Zephaniah 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzasamula dzanja langa kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu. Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za Baala pa malo ano. Palibe aliyense amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo a ndidzaononga otsala a Baala kuwacotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;