Zephaniah 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho zoŵeta zizidzagona kumeneko chimodzimodzinso nyama zonse zakuthengo. Adembo ndi akanungu azidzagona pa makapotolosi ake. Akadzidzi azidzalira pa windo, ndipo makwangwala azidzakhala pa bwalo lake. Mitengo yake yamkungudza adzaisadza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko, pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse. Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu adzakhala pa nsanamira zake. Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera, mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha, nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pace; nyama zonse za mitundu mitundu; ndi bvuo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zace; adzayimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala cipasuko; pakuti anagadamula nchito yace ya mkungudza.