Zephaniah 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munacita ciweruzo cace; funani cilungamo, funani cifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.