Zephaniah 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikulumbira kuti, Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo wa Israele, Amowabu adzaonongedwa ngati anthu a ku Sodomu, Aamoni adzaonongedwa ngati anthu a ku Gomora. Malowo adzakhala ngati dera la zitsamba za khwisa ndi la nkhuti za mchere, dziko lachipululu mpaka muyaya. Otsala mwa anthu anga adzafunkha malowo. Opulumuka a mtundu wanga adzalandira malowo ngati dziko lao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, pali Ine Wamoyo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, “Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu, Amoni adzasanduka ngati Gomora; malo a zomeramera ndi maenje a mchere, dziko la bwinja mpaka muyaya. Anthu anga otsala adzawafunkha; opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pocuruka khwisa ndi maenje a mcere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala amtundu wa anthu anga adzawalandira akhale colowa cao.